-
Danieli 10:8-10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Choncho ndinatsala ndekha ndipo nditaona masomphenya odabwitsawa, mphamvu zonse zinandithera. Nkhope yanga imene inkaoneka yolemekezeka inasintha kwambiri, moti ndinalibenso mphamvu.+ 9 Kenako ndinamva munthu uja akulankhula. Koma nditamva kuti akulankhula, ndinagona pansi chafufumimba nʼkugona tulo tofa nato.+ 10 Ndiyeno ndinamva dzanja likundikhudza+ ndipo linandigwedeza kuti ndidzuke. Nditadzuka ndinagwada nʼkugwira pansi ndi manja anga.
-