-
1 Samueli 22:22, 23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Ndiyeno Davide anauza Abiyatara kuti: “Tsiku lomwe lija+ nditangoona kuti Doegi wa ku Edomu aliko, ndinadziwa kuti akauza Sauli. Ineyo ndi amene ndachititsa kuti anthu onse amʼnyumba ya bambo ako aphedwe. 23 Koma iwe khala ndi ine ndipo usachite mantha. Chifukwa aliyense amene akufunafuna moyo wako akufunafunanso moyo wanga, ndipo ndikuteteza.”+
-