-
2 Samueli 3:26, 27Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
26 Ndiyeno Yowabu anachoka nʼkumusiya Davide ndipo anatuma anthu kuti akamubweze Abineri. Anthuwo anamupeza Abineri pachitsime cha Sira, koma Davide sanadziwe chilichonse. 27 Abineri atabwerera ku Heburoni,+ Yowabu anamʼtengera pambali kugeti kuti alankhulane naye pa awiri. Koma kumeneko anamubaya pamimba moti anafa.+ Anamupha chifukwa choti anapha Asaheli, mchimwene wake wa Yowabuyo.+
-