-
1 Mafumu 8:46-50Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
46 Anthu anu akakuchimwirani (popeza palibe munthu amene sachimwa)+ inu nʼkuwakwiyira kwambiri ndiponso kuwapereka kwa adani, adani awowo nʼkuwatenga kupita nawo kudziko lakutali kapena lapafupi,+ 47 ndiyeno iwo nʼkuzindikira kulakwa kwawo mʼdziko limene anawatengeralo+ nʼkulapa,+ ndiponso akapempha chifundo kwa inu mʼdziko la adani awowo+ nʼkunena kuti, ‘Tachimwa, talakwitsa ndiponso tachita zinthu zoipa,’+ 48 nʼkubwerera kwa inu ndi mtima wawo wonse ndi moyo wawo wonse,+ mʼdziko la adani awo amene anawagwira ndiponso akapemphera kwa inu atayangʼana kudziko lawo limene munapatsa makolo awo, mzinda umene mwasankha komanso nyumba ya dzina lanu imene ndamanga,+ 49 inuyo, kumwamba kumene mumakhalako,+ mumve pemphero lawo ndi pempho lawo lopempha chifundo ndipo muonetsetse kuti chilungamo chachitika kwa iwo. 50 Mukhululukire anthu anu amene anakuchimwirani. Muwakhululukire zimene anakulakwirani. Muchititse kuti adani awo amene anawatenga azikhudzidwa mtima ndipo aziwamvera chisoni,+
-
-
Danieli 9:7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Inu Yehova ndinu wolungama, koma ifeyo tadzibweretsera manyazi* ngati mmene zilili lero. Manyazi agwira amuna a mu Yuda, anthu a ku Yerusalemu ndi anthu onse a ku Isiraeli, amene ali pafupi ndiponso amene ali kutali, kumayiko onse amene munawabalalitsirako chifukwa choti anakuchitirani zinthu zosakhulupirika.+
-