-
Nehemiya 1:6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Chonde, tsegulani maso anu ndi kutchera khutu kuti mumve pemphero la ine mtumiki wanu limene ndikupemphera kwa inu lero. Masana ndi usiku+ ndikumapempherera atumiki anu, Aisiraeli. Pochita zimenezi ndikuvomereza machimo a Aisiraeli amene tinakuchimwirani. Tonse tinachimwa, ine limodzi ndi nyumba ya bambo anga.+
-
-
Danieli 9:5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Ife tachimwa, tachita zinthu zolakwika komanso zoipa ndipo takupandukirani.+ Tapatuka nʼkusiya kutsatira malamulo ndi zigamulo zanu.
-