-
Deuteronomo 30:1-3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
30 “Mawu onsewa akadzakwaniritsidwa pa inu, madalitso ndi matemberero amene ndaika pamaso panu,+ ndipo mukadzawakumbukira*+ muli ku mitundu yonse kumene Yehova Mulungu wanu adzakubalalitsireni,+ 2 inu nʼkubwerera kwa Yehova Mulungu wanu+ komanso kumvera mawu ake ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, mogwirizana ndi zonse zimene ndikukulamulani lero, inuyo ndi ana anu,+ 3 Yehova Mulungu wanu adzabweza kwawo anthu a mtundu wanu amene anagwidwa nʼkupita kudziko lina,+ ndipo adzakuchitirani chifundo+ nʼkukusonkhanitsaninso pamodzi kuchokera pakati pa anthu onse kumene Yehova Mulungu wanu anakubalalitsirani.+
-
-
Danieli 9:2, 3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 mʼchaka choyamba cha ulamuliro wake, ineyo Danieli ndinazindikira chiwerengero cha zaka zimene zinatchulidwa mʼmawu amene Yehova anauza mneneri Yeremiya, kuti Yerusalemu adzakhala bwinja+ kwa zaka 70.+ Ndinazindikira zimenezi nditawerenga mʼmabuku.* 3 Choncho ndinayangʼana kwa Yehova Mulungu woona ndipo ndinapemphera momuchonderera, ndinasala kudya,+ ndinavala ziguduli komanso kudzithira phulusa.
-