-
1 Mafumu 10:16, 17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Mfumu Solomo anapanga zishango 200 zikuluzikulu za golide wosakaniza ndi zitsulo zina.+ (Chishango chilichonse anachikuta ndi golide wolemera masekeli* 600.)+ 17 Anapanganso zishango 300 zingʼonozingʼono* za golide wosakaniza ndi zitsulo zina. (Chishango chilichonse anachikuta ndi golide wolemera ma mina* atatu.) Kenako mfumuyo inaika zishangozi mʼnyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni.+
-
-
1 Mafumu 14:25-28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Mʼchaka cha 5 cha Mfumu Rehobowamu, Sisaki mfumu ya Iguputo+ anaukira Yerusalemu.+ 26 Iye anatenga chuma chamʼnyumba ya Yehova ndi chuma chamʼnyumba ya mfumu.+ Anatenga chilichonse kuphatikizapo zishango zonse zagolide zimene Solomo anapanga.+ 27 Choncho Mfumu Rehobowamu anapanga zishango zakopa* mʼmalomwake ndipo anazipereka kwa akulu a asilikali* olondera pakhomo la nyumba ya mfumu kuti aziziyangʼanira. 28 Nthawi iliyonse imene mfumuyo ikupita kunyumba ya Yehova, asilikaliwo ankanyamula zishangozo ndipo kenako ankazibwezera kuchipinda cha alonda.
-