-
Danieli 10:1Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Mʼchaka chachitatu cha ulamuliro wa Mfumu Koresi+ ya Perisiya, Mulungu anamuululira nkhani inayake Danieli, amene ankadziwikanso ndi dzina lakuti Belitesazara.+ Nkhani imene anauzidwayo inali yoona ndipo inali yokhudza nkhondo yaikulu. Danieli anamvetsa nkhani imeneyi ndipo anathandizidwa kumvetsa zinthu zimene anaonazo.
-