-
Levitiko 27:34Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
34 Amenewa ndi malamulo amene Yehova anapatsa Mose paphiri la Sinai+ kuti apereke kwa Aisiraeli.
-
-
Numeri 36:13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Amenewa ndi malamulo ndi zigamulo za Yehova, zimene anapereka kwa Aisiraeli kudzera mwa Mose ku Yeriko, mʼchipululu cha Mowabu, pafupi ndi mtsinje wa Yorodano.+
-
-
Deuteronomo 12:1Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 “Awa ndi malangizo ndi zigamulo zimene muyenera kutsatira mosamala, masiku onse amene mudzakhale mʼdziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu adzakupatseni kuti likhale lanu.
-
-
Nehemiya 9:34Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
34 Mafumu athu, akalonga athu, ansembe athu ndi makolo athu sanatsatire Chilamulo chanu ndipo sanamvere malamulo anu kapena zikumbutso zanu zowachenjeza.
-