19 Panalibe mzinda winanso umene unagwirizana za mtendere ndi Aisiraeli, kupatulapo Ahivi a ku Gibiyoni.+ Aisiraeli anamenyana ndi mizinda ina yonse nʼkuigonjetsa.+
7 Kenako Melatiya wa ku Gibiyoni+ ndi Yadoni wa ku Meronoti anapitiriza kuchokera pamene Yoyada ndi Mesulamu analekezera. Amenewa anali amuna a ku Gibiyoni ndi Mizipa+ amene anali pansi pa ulamuliro wa bwanamkubwa wakutsidya la Mtsinje.*+