-
Nehemiya 10:38, 39Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
38 Wansembe, mwana wamwamuna wa Aroni, azikhala ndi Alevi pamene iwo akutolera chakhumi. Aleviwo azipereka gawo limodzi pa magawo 10 a chakhumicho kunyumba ya Mulungu wathu+ kuzipinda* za nyumba yosungira katundu. 39 Chifukwa Aisiraeli ndi Alevi ayenera kubweretsa zopereka+ zambewu, vinyo watsopano ndi mafuta+ kuzipinda zosungira katundu.* Kumeneku nʼkumene kuli ziwiya zakumalo opatulika, ansembe amene amatumikira, alonda apageti ndiponso oimba. Sitidzanyalanyaza nyumba ya Mulungu wathu.+
-