-
1 Mafumu 4:29Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
29 Mulungu anapatsa Solomo nzeru, luso lozindikira komanso mtima womvetsa zinthu zambirimbiri ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja.+
-
-
Mlaliki 2:26Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
26 Munthu amene amasangalatsa Mulungu, Mulunguyo amamʼpatsa nzeru ndi kudziwa zinthu komanso amamuchititsa kuti azisangalala.+ Koma munthu wochimwa amamʼpatsa ntchito yotuta ndi kusonkhanitsa zinthu kuti azipereke kwa munthu amene amasangalatsa Mulungu woona.+ Zimenezinso nʼzachabechabe, zili ngati kuthamangitsa mphepo.
-