-
Yobu 2:1-3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Pambuyo pa zimenezi, linafika tsiku limene ana a Mulungu woona*+ anapita kukaonekera pamaso pa Yehova,+ ndipo Satana nayenso anapita kukaonekera pamaso pa Yehova.+
2 Kenako Yehova anafunsa Satana kuti: “Kodi ukuchokera kuti iwe?” Satanayo anayankha Yehova kuti: “Ndimazungulira mʼdziko lapansi komanso kuyendayendamo.”+ 3 Ndiyeno Yehova anafunsanso Satana kuti: “Kodi mtima wako uli pa mtumiki wanga Yobu? Padziko lapansi palibe wina wofanana naye. Iye ndi munthu wokhulupirika amene amachita zoyenera,*+ amaopa Mulungu ndiponso amapewa zoipa. Iye akupitirizabe kukhala wokhulupirika+ ngakhale kuti iweyo ukufuna kuti ndimuwononge*+ popanda chifukwa.”
-