-
2 Samueli 10:6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Patapita nthawi, Aamoni anaona kuti akhala ngati chinthu chonunkha kwa Davide. Choncho anatumiza anthu kuti akalembe ganyu Asiriya a ku Beti-rehobu+ ndi Asiriya a ku Zoba+ ndipo onse pamodzi analipo asilikali 20,000 oyenda pansi. Anapitanso kwa mfumu ya ku Maaka+ nʼkulemba ganyu amuna 1,000 komanso ku Isitobu amuna 12,000.+
-
-
Yesaya 7:2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Ndiyeno kunyumba ya Davide kunapita uthenga wakuti: “Dziko la Siriya lachita mgwirizano ndi dziko la Efuraimu.”
Choncho mtima wa Ahazi ndi wa anthu ake unayamba kunjenjemera, ngati mitengo ya mʼnkhalango imene ikugwedezeka ndi mphepo.
-
-
Yesaya 7:5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Chifukwa Siriya ndi Efuraimu ndiponso mwana wa Remaliya akukonzera zoipa ndipo anena kuti:
-