-
Yoswa 4:5-7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Ndipo anawauza kuti: “Dutsani kutsogolo kwa Likasa la Yehova Mulungu wanu, mukafike pakati pa mtsinje wa Yorodano. Aliyense akanyamule mwala umodzi paphewa pake, mogwirizana ndi chiwerengero cha mafuko a Aisiraeli. 6 Miyalayo idzakhala chizindikiro kwa inu. Ana anu* akamadzafunsa mʼtsogolo muno kuti, ‘Kodi miyalayi ndi ya chiyani?’+ 7 Muzidzawauza kuti: ‘Nʼchifukwa chakuti madzi amumtsinje wa Yorodano anagawikana chifukwa cha likasa+ la pangano la Yehova. Likasalo likudutsa mumtsinje wa Yorodano, madzi a mtsinjewo anagawikana. Miyalayi ndi yoti izikumbutsa Aisiraeli zimenezo mpaka kalekale.’”+
-