15 Choncho ntchito yomanga mpanda inatha pa tsiku la 25 la mwezi wa Eluli ndipo inatenga masiku 52.
16 Adani athu onse atangomva zimenezi komanso anthu a mitundu ina yotizungulira ataona, anachita manyazi kwambiri+ ndipo anazindikira kuti ntchitoyi yatheka chifukwa cha Mulungu wathu.