26 Ine ndikulamula kuti mʼzigawo zonse za ufumu wanga, anthu azinjenjemera chifukwa cha mantha pamaso pa Mulungu wa Danieli.+ Chifukwa iye ndi Mulungu wamoyo ndipo adzakhalapo mpaka kalekale. Ufumu wake sudzawonongedwa komanso ulamuliro wake udzakhalapo kwamuyaya.+