-
Salimo 119:91Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
91 Ntchito zanu zilipobe mpaka pano chifukwa cha zigamulo zanu,
Chifukwa zonsezo zimakutumikirani.
-
-
Yeremiya 31:35, 36Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
35 Yehova amene amapereka dzuwa kuti liziwala masana,
Amene amaika malamulo oti mwezi ndi nyenyezi ziziwala usiku,
Amene amavundula nyanja
Kuti mafunde ake achite phokoso,
Amene dzina lake ndi Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, wanena kuti:+
36 “‘Ngati malamulo amenewa angalephere kugwira ntchito yake,
Ndiye kutinso mbadwa za Isiraeli zingasiye kukhala mtundu, umene umakhala pamaso panga nthawi zonse,’ akutero Yehova.”+
-