-
2 Mbiri 26:16-18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Koma atangokhala wamphamvu, mtima wake unayamba kudzikuza mpaka kufika pomʼpweteketsa. Iye anachita zosakhulupirika kwa Yehova Mulungu wake ndipo anapita mʼkachisi wa Yehova kukapereka nsembe zofukiza paguwa lansembe.+ 17 Nthawi yomweyo wansembe Azariya komanso ansembe ena a Yehova olimba mtima okwanira 80, anamutsatira. 18 Iwo anapita pamene panali Mfumu Uziya kukamuletsa. Anamuuza kuti: “Mfumu Uziya, si zoyenera kuti inuyo mupereka nsembe zofukiza kwa Yehova.+ Ansembe okha ndi amene ayenera kupereka nsembe zofukiza chifukwa ndi mbadwa za Aroni+ ndipo anayeretsedwa. Tulukani mʼnyumba yopatulikayi popeza mwachita zosakhulupirika ndipo zimenezi sizikubweretserani ulemerero wochokera kwa Yehova Mulungu.”
-