-
Salimo 38:22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Bwerani mwamsanga mudzandithandize,
Inu Yehova, amene mumandipulumutsa.+
-
-
Salimo 70:1-5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
70 Inu Mulungu, ndipulumutseni,
Inu Yehova, ndithandizeni mofulumira.+
2 Amene akufuna kuchotsa moyo wanga
Achititsidwe manyazi komanso anyozeke.
Amene akusangalala ndi tsoka langa
Abwerere mwamanyazi.
3 Onse amene akunena kuti: “Eyaa! Eyaa!”
Abwezedwe mwamanyazi.
4 Koma amene akufunafuna inu,
Akondwere ndi kusangalala chifukwa choti akudziwani.+
Amene amasangalala ndi njira imene mumapulumutsira anthu, nthawi zonse azinena kuti:
“Mulungu alemekezeke.”
-