Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • Deuteronomo 15:7, 8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Ngati mmodzi mwa abale anu wasauka pakati panu, mu umodzi mwa mizinda yanu mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, musamamuumire mtima kapena kumuumitsira dzanja lanu.+ 8 Koma muzithandiza mʼbale wanuyo mowolowa manja,+ ndipo mulimonse mmene zingakhalire, muzimukongoza* chilichonse chimene akufuna kapena chimene akusowa.

  • Salimo 112:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  9 Iye wagawira ena mowolowa manja, wapereka kwa anthu osauka.+

      צ [Tsade]

      Chilungamo chake chidzakhalapo mpaka kalekale.+

      ק [Qoph]

      Mphamvu zake zidzawonjezeka* chifukwa cha ulemerero.

  • Miyambo 14:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Munthu amene amanyoza mnzake ndiye kuti akuchimwa,

      Koma wosangalala ndi munthu amene amakomera mtima anthu onyozeka.+

  • Miyambo 22:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  9 Munthu wowolowa manja* adzadalitsidwa,

      Chifukwa amagawana chakudya chake ndi anthu osauka.+

Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • tumizirani
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • zachinsinsi
  • JW.ORG
  • Lowani
tumizirani