-
Esitere 1:10-12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Pa tsiku la 7, mtima wa mfumu utasangalala chifukwa chomwa vinyo, mfumuyo inauza Mehumani, Bizita, Haribona,+ Bigita, Abagata, Zetara ndi Karikasi, nduna 7 zomwe zinkatumikira Mfumu Ahasiwero, 11 kuti akatenge Mfumukazi Vasiti nʼkubwera naye kwa mfumu atavala duku lachifumu, kuti anthu onse ndi akalonga aone kukongola kwake, chifukwa analidi wokongola kwambiri. 12 Koma Mfumukazi Vasiti anakana atauzidwa ndi nduna zapanyumba ya mfumu kuti mfumu yalamula kuti apite. Zitatero mfumuyo inakwiya kwambiri ndipo inapsa mtima.
-