-
1 Mafumu 4:29-31Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
29 Mulungu anapatsa Solomo nzeru, luso lozindikira komanso mtima womvetsa zinthu zambirimbiri ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja.+ 30 Nzeru za Solomo zinaposa nzeru za anthu onse a Kumʼmawa komanso nzeru zonse za ku Iguputo.+ 31 Iye anali wanzeru kuposa munthu aliyense. Anali wanzeru kuposa Etani+ mbadwa ya Zera ndiponso Hemani,+ Kalikoli+ ndi Darida ana a Maholi moti anatchuka mʼmitundu yonse yozungulira.+
-