-
1 Mafumu 9:17-19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Solomo anamanganso Gezeri, Beti-horoni Wakumunsi,+ 18 Baalati+ ndi Tamara mʼchipululu cha mʼdzikolo. 19 Anamanganso mizinda yake yonse yosungirako zinthu, mizinda yosungirako magaleta,+ mizinda ya amuna okwera pamahatchi ndiponso zilizonse zimene iye anafuna kumanga ku Yerusalemu, ku Lebanoni ndi mʼmadera onse amene ankalamulira.
-
-
2 Mbiri 9:15, 16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Mfumu Solomo anapanga zishango 200 zikuluzikulu za golide wosakaniza ndi zitsulo zina.+ (Chishango chilichonse anachikuta ndi golide wolemera masekeli* 600.)+ 16 Anapanganso zishango 300 zingʼonozingʼono* za golide wosakaniza ndi zitsulo zina. (Chishango chilichonse anachikuta ndi golide wolemera ma mina* atatu.) Kenako mfumuyo inaika zishangozi mʼnyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni.+
-