-
Yesaya 32:14, 15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Chifukwa nsanja yokhala ndi mpanda wolimba yasiyidwa.
Mzinda waphokoso wasiyidwa.+
Ofeli+ ndi nsanja ya mlonda zasanduka chipululu mpaka kalekale.
Zasanduka malo amene abulu amʼtchire akusangalalako,
Komanso malo odyetserako ziweto,+
15 Mpaka mzimu utatsanulidwa pa ife kuchokera kumwamba,+
Ndiponso chipululu chitakhala munda wa zipatso,
Komanso munda wa zipatsowo utayamba kuoneka ngati nkhalango.+
-
-
Yesaya 60:21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Anthu ako onse adzakhala olungama.
Adzatenga dzikoli kukhala lawo mpaka kalekale.
-