9 Kwera paphiri lalitali,
Iwe mkazi amene ukubweretsa uthenga wabwino wonena za Ziyoni.+
Fuula mwamphamvu,
Iwe mkazi amene ukubweretsa uthenga wabwino wonena za Yerusalemu.
Fuula, usachite mantha.
Lengeza kumizinda ya ku Yuda kuti: “Mulungu wanu ali nanu.”+