Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • Yesaya 44:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Fuulani mosangalala kumwamba inu,

      Chifukwa Yehova wachita zimenezi.

      Fuulani posonyeza kupambana, inu malo otsika kwambiri a dziko lapansi.

      Mapiri inu, fuulani mosangalala,+

      Iwe nkhalango ndi inu mitengo yonse imene ili mmenemo,

      Chifukwa Yehova wawombola Yakobo,

      Ndipo wasonyeza kukongola kwake pa Isiraeli.”+

  • Yesaya 61:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  3 Kuti ndisamalire anthu onse amene akulirira Ziyoni,

      Kuti ndiwapatse nsalu yovala kumutu mʼmalo mwa phulusa,

      Kuti ndiwapatse mafuta kuti azisangalala mʼmalo molira,

      Kuti ndiwapatse chovala choti azivala ponditamanda mʼmalo mokhala otaya mtima.

      Ndipo iwo adzatchedwa mitengo ikuluikulu ya chilungamo,

      Yodzalidwa ndi Yehova kuti iyeyo alemekezedwe.*+

  • Yeremiya 31:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 “Pa nthawi imeneyo, anamwali,

      Anyamata ndiponso amuna achikulire, adzavina pamodzi mosangalala.+

      Kulira kwawo ndidzakusandutsa chisangalalo.+

      Ndidzawatonthoza ndipo ndidzachititsa kuti akhale osangalala mʼmalo mokhala achisoni.+

Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • tumizirani
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • zachinsinsi
  • JW.ORG
  • Lowani
tumizirani