-
Mika 7:16, 17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Anthu a mitundu ina adzaona zodabwitsazo ndipo adzachita manyazi ngakhale kuti ndi amphamvu.+
Iwo adzagwira pakamwa,
Ndipo makutu awo adzagontha.
17 Adzanyambita fumbi ngati njoka.+
Ngati nyama zokwawa, adzatuluka akunjenjemera mʼmalo awo obisalamo.
Adzabwera kwa Yehova Mulungu akuchita mantha,
Ndipo adzayamba kukuopani.”+
-