-
Yeremiya 29:14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Ndidzakulolani kuti mundipeze,’+ akutero Yehova. ‘Ndidzasonkhanitsa anthu amene anagwidwa nʼkutengedwa kupita kumayiko ena kuchokera mʼmitundu yonse ndi kumalo onse kumene ndinakubalalitsirani,’+ akutero Yehova. ‘Kenako ndidzakubwezeretsani kumalo amene ndinakuchotsani pa nthawi imene ndinakupititsani ku ukapolo.’+
-
-
Hoseya 6:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Komanso, inu anthu a ku Yuda, nthawi yoti mukololedwe yakhazikitsidwa.
Ine ndidzasonkhanitsanso anthu anga amene anatengedwa kupita kudziko lina.”+
-