Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • Deuteronomo 31:16, 17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Tsopano Yehova anauza Mose kuti: “Iweyo watsala pangʼono kufa,* ndipo anthu awa adzakhala osakhulupirika kwa ine ndipo adzayamba kulambira milungu yachilendo imene ili mʼdziko limene akupita.+ Iwo adzandisiya+ nʼkuphwanya pangano limene ndinapangana nawo.+ 17 Pa nthawi imeneyo mkwiyo wanga udzawayakira+ ndipo ndidzawasiya+ nʼkuwabisira nkhope yanga+ mpaka atawonongedwa.+ Ndiyeno akadzakumana ndi masoka komanso mavuto ambiri adzanena kuti, ‘Masoka amenewatu akutigwera chifukwa chakuti Mulungu wathu sali pakati pathu.’+

  • Deuteronomo 32:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Choncho iye anati, ‘Ndiwabisira nkhope yanga,+

      Ndione kuti ziwathera bwanji.

      Chifukwa iwo ndi mʼbadwo wokonda zoipa,+

      Ana osakhulupirika.+

  • Yesaya 57:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Ine ndinakwiya chifukwa cha machimo amene ankachita pofuna kupeza phindu mwachinyengo,+

      Choncho ndinamulanga, ndinabisa nkhope yanga ndipo ndinakwiya.

      Koma iye anapitiriza kuyenda ngati wopanduka,+ ankangotsatira zofuna za mtima wake.

  • Ezekieli 39:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Anthu a mitundu ina adzadziwa kuti a nyumba ya Isiraeli anatengedwa kupita ku ukapolo chifukwa cha zolakwa zawo, popeza anandichitira zinthu mosakhulupirika.+ Choncho ine ndinawabisira nkhope yanga+ nʼkuwapereka kwa adani awo+ ndipo onse anaphedwa ndi lupanga.

  • Mika 3:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Pa nthawiyo adzafuulira Yehova kuti awathandize,

      Koma sadzawayankha.

      Adzawabisira nkhope yake pa nthawi imeneyo,+

      Chifukwa cha zochita zawo zoipa.+

Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • tumizirani
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • zachinsinsi
  • JW.ORG
  • Lowani
tumizirani