-
Yesaya 30:27Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
27 Taonani! Dzina la Yehova likubwera kuchokera kutali.
Likubwera ndi mkwiyo wake woyaka moto ndiponso mitambo yolemera.
Iye akulankhula mwaukali,
Ndipo lilime lake lili ngati moto wowononga.+
-
-
Yesaya 31:8, 9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Msuri adzaphedwa ndi lupanga, koma osati la munthu.
Lupanga lidzamudya, koma osati la munthu.+
Iye adzathawa chifukwa cha lupangalo
Ndipo anyamata ake adzagwiritsidwa ntchito yaukapolo.
9 Thanthwe lake lidzachoka chifukwa cha mantha,
Ndipo akalonga ake adzachita mantha chifukwa cha chizindikiro,” akutero Yehova,
Amene kuwala kwake kuli mu Ziyoni* ndiponso amene ngʼanjo yake ili mu Yerusalemu.
-