-
Yesaya 56:6, 7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Ndipo alendo amene abwera kwa Yehova kuti amutumikire,
Kuti azikonda dzina la Yehova+
Ndiponso kuti akhale atumiki ake,
Onse amene amasunga Sabata ndipo salidetsa
Komanso amene amatsatira pangano langa,
7 Nawonso ndidzawabweretsa kuphiri langa loyera+
Ndipo ndidzawachititsa kuti asangalale mʼnyumba yanga yopemphereramo.
Nsembe zawo zopsereza zathunthu ndi nsembe zawo zina ndidzazilandira paguwa langa lansembe.
Chifukwa nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo anthu a mitundu yonse.”+
-