13 Kodi ndikupatse umboni wotani,
Kapena kodi ndingakuyerekezere ndi chiyani, iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu?
Kodi ndikufananitse ndi chiyani kuti ndikutonthoze, namwali iwe, mwana wamkazi wa Ziyoni?
Chifukwa kuwonongeka kwako kwafalikira ngati kukula kwa nyanja.+ Ndani angakuchiritse?+