-
Yoswa 10:29, 30Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
29 Zitatero, Yoswa ndi Aisiraeli onse amene anali naye anachoka ku Makeda nʼkupita kukamenyana ndi anthu a ku Libina.+ 30 Yehova anaperekanso mzindawo ndi mfumu yake mʼmanja mwa Isiraeli.+ Choncho Aisiraeli anapha anthu onse amumzindawo ndi lupanga, ndipo anaonetsetsa kuti pasakhale wopulumuka. Mfumu ya ku Libina anaichita zofanana ndi zomwe anaichita mfumu ya ku Yeriko.+
-
-
2 Mafumu 8:22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Koma Aedomu anapitirizabe kugalukira Yuda mpaka lero. Pa nthawi imeneyi mʼpamenenso Libina+ anagalukira Yuda.
-
-
2 Mafumu 19:8-13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Rabisake atamva kuti mfumu ya Asuri yachoka ku Lakisi+ anabwerera kwa mfumuyo ndipo anaipeza ikumenyana ndi Libina.+ 9 Mfumuyo inamva zokhudza Tirihaka mfumu ya Itiyopiya kuti: “Wabwera kudzamenyana nanu.” Choncho inatumizanso uthenga+ kwa Hezekiya wakuti: 10 “Mukauze Hezekiya mfumu ya Yuda kuti, ‘Mulungu wako amene ukumudalira asakunamize, ponena kuti: “Yerusalemu saperekedwa mʼmanja mwa mfumu ya Asuri.”+ 11 Iweyo wamva zimene mafumu a Asuri anachitira mayiko onse, kuti anawawononga.+ Ndiye iweyo ukuona ngati upulumuka? 12 Kodi milungu ya mitundu imene makolo anga anaiwononga inawapulumutsa? Kodi inapulumutsa Gozani, Harana,+ Rezefi ndi anthu a ku Edeni amene anali ku Tela-sara? 13 Ili kuti mfumu ya Hamati, mfumu ya Aripadi ndiponso mfumu ya mzinda wa Sefaravaimu, wa Hena ndi wa Iva?’”+
-