-
2 Mafumu 19:14-19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Hezekiya anatenga makalatawo mʼmanja mwa anthuwo nʼkuwawerenga. Kenako iye anapita nawo kunyumba ya Yehova nʼkuwatambasula pamaso pa Yehova.+ 15 Ndiyeno Hezekiya anayamba kupemphera+ kwa Yehova kuti: “Inu Yehova Mulungu wa Isiraeli wokhala pamwamba* pa akerubi,+ inu nokha ndinu Mulungu woona wa maufumu onse apadziko lapansi.+ Inuyo munapanga kumwamba ndi dziko lapansi. 16 Tcherani khutu lanu, inu Yehova, mumve.+ Tsegulani maso anu,+ inu Yehova, muone. Imvani mawu amene Senakeribu watumiza onyoza Mulungu wamoyo. 17 Nʼzoonadi Yehova, kuti mafumu a Asuri awononga mayiko ndi anthu a mʼmayikowo.+ 18 Aponya milungu yawo pamoto, chifukwa sinali milungu,+ koma ntchito ya manja a anthu,+ mitengo ndi miyala. Nʼchifukwa chake anatha kuiwononga. 19 Tsopano inu Yehova Mulungu wathu, chonde tipulumutseni mʼmanja mwake, kuti maufumu onse apadziko lapansi adziwe kuti inu nokha Yehova, ndinu Mulungu.”+
-