-
2 Mafumu 19:20, 21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Ndiyeno Yesaya mwana wa Amozi anatumiza uthenga kwa Hezekiya, wakuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ndamva pemphero lako+ lokhudza Senakeribu mfumu ya Asuri.+ 21 Awa ndi mawu otsutsana naye amene Yehova wanena:
“Namwali, mwana wamkazi wa Ziyoni, wakunyoza ndipo wakunyodola.
Mwana wamkazi wa Yerusalemu wakupukusira mutu.
-