-
2 Mafumu 19:29-31Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
29 Ichi chidzakhala chizindikiro chanu:* Chaka chino mudya mbewu zimene zamera zokha. Mʼchaka chachiwiri mudzadya mbewu zophuka kuchokera ku mbewu zimenezi.+ Koma mʼchaka chachitatu, mudzadzala mbewu nʼkukolola ndipo mudzalima minda ya mpesa nʼkudya zipatso zake.+ 30 Anthu amʼnyumba ya Yuda amene adzapulumuke, amene adzatsale,+ adzakhala ngati mitengo imene yazika mizu pansi nʼkubereka zipatso zambiri. 31 Chifukwa anthu otsala adzachokera ku Yerusalemu ndipo opulumuka adzachokera kuphiri la Ziyoni. Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzachita zimenezi modzipereka kwambiri.+
-