-
Yoweli 2:18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Ndiyeno Yehova adzachitira nsanje dziko lake,
Ndipo adzachitira chifundo anthu ake.+
-
-
Zekariya 1:14, 15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Ndiyeno mngelo amene ankalankhula nane uja anandiuza kuti: “Fuula kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Ndatsimikiza mtima kuti nditeteze Yerusalemu ndi Ziyoni.+ 15 Ndakwiyira kwambiri anthu a mitundu ina amene akukhala mosatekeseka.+ Ndawakwiyira chifukwa chakuti ine ndinangokwiyira anthu anga pangʼono,+ koma anthu amenewa anakulitsa kwambiri mavuto a anthu angawo.”’+
-