-
Ezara 4:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Adani a Yuda ndi Benjamini+ atamva kuti anthu amene anabwera kuchokera ku ukapolo+ akumangira kachisi Yehova Mulungu wa Isiraeli, 2 nthawi yomweyo anapita kwa Zerubabele ndi atsogoleri a nyumba za makolo nʼkukawauza kuti: “Bwanji tizimanga limodzi chifukwa ifeyo, mofanana ndi inuyo, timalambira* Mulungu wanu.+ Komanso timapereka nsembe kwa iye kuyambira mʼmasiku a Esari-hadoni+ mfumu ya Asuri, yemwe anatibweretsa kuno.”+
-