Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • Deuteronomo 28:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Koma mukapanda kumvera mawu a Yehova Mulungu wanu poonetsetsa kuti mukutsatira malamulo ake onse ndi malangizo ake amene ndikukupatsani lero, mudzatembereredwa ndipo zinthu zoipa zotsatirazi zidzakuchitikirani:+

  • Deuteronomo 29:26, 27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Koma iwo anapita kukatumikira milungu ina ndi kuigwadira, milungu imene sankaidziwa komanso imene sanawalole kuti aziilambira.+ 27 Zitatero mkwiyo wa Yehova unayakira dziko limeneli ndipo analibweretsera matemberero onse amene analembedwa mʼbuku ili.+

  • Yoswa 23:15, 16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Koma mofanana ndi malonjezo onse abwino amene Yehova Mulungu wanu ananena omwe akwaniritsidwa pa inu,+ Yehova adzakwaniritsanso pa inu masoka onse* amene ananena, ndipo adzakufafanizani padziko labwino limene Yehova Mulungu wanu wakupatsanili.+ 16 Mukadzaphwanya pangano la Yehova Mulungu wanu limene anakulamulani, komanso mukadzapita kukatumikira milungu ina ndi kuigwadira, Yehova adzakukwiyirani kwambiri+ ndipo simudzachedwa kutha padziko labwino limene iye anakupatsani.”+

  • 2 Mafumu 23:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Yehova anati: “Yuda nayenso ndidzamʼchotsa pamaso panga+ ngati mmene ndinachotsera Isiraeli+ ndipo ndidzakana mzinda wa Yerusalemu umene ndinausankha, ndi nyumba imene ndinanena kuti, ‘Dzina langa lizikhala kumeneko.’”+

Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • tumizirani
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • zachinsinsi
  • JW.ORG
  • Lowani
tumizirani