-
2 Mbiri 36:10-12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Chakumayambiriro kwa chaka, Mfumu Nebukadinezara inatuma asilikali ake omwe anakamutenga nʼkubwera naye ku Babulo+ limodzi ndi zinthu zabwino zamʼnyumba ya Yehova.+ Komanso Nebukadinezara anasankha Zedekiya, yemwe anali mʼbale wa bambo ake a Yehoyakini, kuti akhale mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu.+
11 Zedekiya+ anayamba kulamulira ali ndi zaka 21 ndipo analamulira zaka 11 ku Yerusalemu.+ 12 Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova Mulungu wake. Ndipo sanadzichepetse pamaso pa mneneri Yeremiya+ yemwe ankalankhula molamulidwa ndi Yehova.
-