-
Yeremiya 26:15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Koma mudziwe kuti mukandipha, inuyo, mzindawu ndi anthu onse amene akukhala mumzindawu mukhala ndi mlandu wa magazi chifukwa chopha munthu wosalakwa. Ndithudi, Yehova ndi amene wandituma kuti ndidzakuuzeni mawu onse amene mwamvawa.”
-
-
Yeremiya 38:8, 9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Choncho Ebedi-meleki anatuluka mʼnyumba ya mfumuyo ndipo anakauza mfumu kuti: 9 “Inu mbuyanga mfumu, zimene anthu awa achitira mneneri Yeremiya ndi zoipa. Iwo amuponya mʼchitsime ndipo afera momwemo chifukwa cha njala, popeza mkate watheratu mumzindawu.”+
-