-
Yesaya 66:16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Yehova adzapereka chiweruzo pogwiritsa ntchito moto,
Inde adzagwiritsa ntchito lupanga lake poweruza anthu onse,
Ndipo anthu ophedwa ndi Yehova adzakhala ambiri.
-
-
Yeremiya 25:17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Choncho ndinatenga kapu imene inali mʼdzanja la Yehova ndipo ndinamwetsa mitundu yonse imene Yehova ananditumizako. Mitunduyo ndi iyi:+
-
-
Zefaniya 3:8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Yehova wanena kuti: ‘Choncho pitirizani kundiyembekezera,*+
Mpaka tsiku limene ndidzanyamuke kuti ndikatenge zinthu za anthu omwe ndawagonjetsa.*
Chiweruzo changa ndi choti ndisonkhanitse mitundu ya anthu, ndisonkhanitse maufumu,
Kuti ndiwasonyeze mkwiyo wanga, ndithu mkwiyo wanga wonse woyaka moto,+
Chifukwa moto wa mkwiyo wanga udzawotcheratu dziko lonse lapansi.+
-