-
Numeri 21:13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Atasamuka kumeneko anakamanga msasa mʼdera la chigwa cha Arinoni, mʼchipululu chochokera kumalire a dziko la Aamori. Chigwa cha Arinoni+ chinali malire pakati pa dziko la Mowabu ndi la Aamori.
-
-
Yoswa 13:8, 9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Mose mtumiki wa Yehova anapereka cholowa kwa hafu ina ya fuko la Manase, kwa fuko la Rubeni ndi kwa fuko la Gadi, kutsidya lakumʼmawa kwa mtsinje wa Yorodano.+ 9 Cholowa chawo chinayambira kumzinda wa Aroweli+ umene uli mʼmbali mwa chigwa cha Arinoni,+ ndiponso mzinda umene uli pakatikati pa chigwacho, kuphatikizapo malo onse okwera a Medeba mpaka kukafika ku Diboni.
-