-
Yeremiya 31:8, 9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Ine ndikuwabweretsa kuchokera kudziko lakumpoto,+
Ndidzawasonkhanitsa pamodzi kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+
Pakati pawo padzakhala anthu amene ali ndi vuto losaona, olumala,+
Azimayi oyembekezera komanso amene atsala pangʼono kubereka,
Onse pamodzi adzabwerera kuno ali chigulu.+
9 Iwo adzabwera akulira.+
Ndidzawatsogolera akadzandipempha kuti ndiwakomere mtima.
Chifukwa ine ndine Bambo ake a Isiraeli ndipo Efuraimu ndi mwana wanga woyamba kubadwa.”+
-