-
Yesaya 1:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Yehova wanena kuti: “Kodi nsembe zanu zambirimbirizo zili ndi phindu lanji kwa ine?+
-
-
Yesaya 66:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Munthu amene akupha ngʼombe yamphongo ali ngati amene akupha munthu.+
Amene akupereka nsembe ya nkhosa ali ngati amene akuthyola khosi la galu.+
Munthu amene akupereka mphatso ali ngati amene akupereka magazi a nkhumba.+
Amene akupereka nsembe yachikumbutso ya lubani+ ali ngati munthu amene akupereka dalitso pogwiritsa ntchito mawu onenerera zamatsenga.*+
Anthuwo asankha njira zawozawo,
Ndipo amasangalala ndi zinthu zonyansa.
-
-
Yeremiya 7:21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Wonjezerani nsembe zanu zopsereza zathunthu pansembe zanu zinazo ndipo muzidye nokha.+
-
-
Amosi 5:21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Ine ndimadana ndi zikondwerero zanu ndipo sindigwirizana nazo,+
Komanso sindisangalala ndi fungo la nsembe zanu zoperekedwa pamisonkhano yanu yapadera.
-