Yesaya 30:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Iwo auza anthu oona masomphenya kuti, ‘Lekani kuona masomphenya,’ Ndipo anthu olosera zamʼtsogolo awauza kuti, ‘Musatiuze masomphenya olondola.+ Mutiuze zinthu zotikomera. Muziona masomphenya abodza.+ Yeremiya 5:31 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 31 Aneneri akulosera zabodza,+Ndipo ansembe akugwiritsa ntchito mphamvu zawo kuti azilamulira ena. Anthu anga nawonso akukonda zimenezi.+ Koma kodi mudzachita chiyani mapeto akadzafika?” Yeremiya 14:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Ndiyeno Yehova anandiyankha kuti: “Aneneriwo akulosera zinthu zabodza mʼdzina langa.+ Ine sindinawatume, kuwalamula kapena kulankhula nawo.+ Maulosi amene akukuuzaniwo ndi masomphenya abodza, maulosi opanda pake ndi chinyengo chamumtima mwawo.+
10 Iwo auza anthu oona masomphenya kuti, ‘Lekani kuona masomphenya,’ Ndipo anthu olosera zamʼtsogolo awauza kuti, ‘Musatiuze masomphenya olondola.+ Mutiuze zinthu zotikomera. Muziona masomphenya abodza.+
31 Aneneri akulosera zabodza,+Ndipo ansembe akugwiritsa ntchito mphamvu zawo kuti azilamulira ena. Anthu anga nawonso akukonda zimenezi.+ Koma kodi mudzachita chiyani mapeto akadzafika?”
14 Ndiyeno Yehova anandiyankha kuti: “Aneneriwo akulosera zinthu zabodza mʼdzina langa.+ Ine sindinawatume, kuwalamula kapena kulankhula nawo.+ Maulosi amene akukuuzaniwo ndi masomphenya abodza, maulosi opanda pake ndi chinyengo chamumtima mwawo.+