-
Yeremiya 16:3, 4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Ponena za ana aamuna ndi ana aakazi amene adzabadwe mʼmalo ano, komanso ponena za amayi ndi abambo amene adzabereke anawo mʼdzikoli, Yehova akuti: 4 ‘Iwo adzafa ndi matenda oopsa+ koma palibe amene adzalire maliro awo kapena kuwaika mʼmanda. Iwo adzakhala ngati manyowa panthaka.+ Adzafa ndi lupanga ndiponso njala.+ Mitembo yawo idzakhala chakudya cha mbalame zamumlengalenga ndi zilombo zakutchire.’
-