18 Zedekiya anayamba kulamulira ali ndi zaka 21 ndipo analamulira zaka 11 ku Yerusalemu. Mayi ake anali a ku Libina ndipo dzina lawo linali Hamutali+ mwana wa Yeremiya. 19 Zedekiya ankachita zoipa pamaso pa Yehova, mogwirizana ndi zonse zimene Yehoyakimu anachita.+