-
2 Mafumu 24:18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Zedekiya anayamba kulamulira ali ndi zaka 21 ndipo analamulira zaka 11 ku Yerusalemu. Mayi ake anali a ku Libina ndipo dzina lawo linali Hamutali+ mwana wa Yeremiya.
-
-
2 Mbiri 36:9, 10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Yehoyakini+ anayamba kulamulira ali ndi zaka 18 ndipo analamulira miyezi itatu ndi masiku 10 ku Yerusalemu. Iye ankachita zoipa pamaso pa Yehova.+ 10 Chakumayambiriro kwa chaka, Mfumu Nebukadinezara inatuma asilikali ake omwe anakamutenga nʼkubwera naye ku Babulo+ limodzi ndi zinthu zabwino zamʼnyumba ya Yehova.+ Komanso Nebukadinezara anasankha Zedekiya, yemwe anali mʼbale wa bambo ake a Yehoyakini, kuti akhale mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu.+
-